Nehemiah 9:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa Inu, ndipo mudachita naye chipangano chakuti zidzukulu zake mudzazipatsa dziko la Akanani, la Ahiti, la Aamori, la Aperezi, la Ayebusi ndi la Agirigasi. Mudachitadi zimene mudalonjezazo, pakuti Inu ndinu olungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu munaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa inu, ndipo munapangana naye pangano lakuti mudzapereka kwa zidzukulu zake dziko la Akanaani Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Inu mwasunga lonjezo lanu chifukwa ndinu wolungama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo munampeza mtima wace wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zace; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.