Numbers 1:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, adasonkhanitsa mpingo wonse. Tsono Aisraele adalembetsa maina ao potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ankalembetsa ndi anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo, mmodzimmodzi,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi waciwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kuchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzi mmodzi.