Numbers 1:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wa Yakobe, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israyeli, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzi mmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;