Numbers 1:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa zidzukulu za Yosefe, ndiye kuti anthu a m'fuko la Efuremu, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efraimu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;