Numbers 1:50 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uike Aleviwo kuti aziyang'anira chihema changa chaumboni, zipangizo zake ndi zonse zimene zili m'menemo. Azinyamula chihemacho, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo azichisamala. Zithando zao azimange pozungulira chihemacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma iwe, uike Alevi asunge Kachisi wa mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula Kachisi, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa Kachisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma iwe, uike Alevi asunge kacisi wa mboni, ndi zipangizo zace zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula kacisi, ndi zipangizo zace zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa kacisi.