Numbers 10:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza Hobaba, mwana wa Reuele Mmidiyani, mpongozi wake uja, kuti, “Tikupita ku malo amene Chauta adati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiyeni tipite limodzi, ndipo tidzakuchitirani zabwino, pakuti Chauta walonjeza Aisraele zinthu zabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reueli Mmidyani mpongozi wa Mose, Ife tirikuyenda kumka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakucitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israyeli zokoma.