Numbers 10:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adanyamuka ku phiri la Chauta, nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi lachipangano la Chauta lidatsogola, nayenda nalo ulendo wa masiku atatu, kuti akapeze malo oti anthu onse aja akapumuleko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayenda kucokera ku phiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la cipangano ca Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.