Numbers 10:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mukukamenya nkhondo m'dziko mwanu ndi adani amene akukuzunzani, nthaŵi imeneyo mulize malipenga ochenjeza, kuti Chauta wanu akukumbukeni, ndipo adzakupulumutsani kwa adani anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kucita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize cokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukila inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.