Numbers 11:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina anthu adadandaula, Chauta alikumva. Chauta atamva zimenezo, adapsa mtima, ndipo moto wa Chautayo udayaka pa anthuwo, nupsereza mbali imodzi ya mahema ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi mota wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku cilekezero ca cigono.