Numbers 11:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndidaatenga pathupi pa anthu onseŵa ndine? Kodi ndidaŵabala ndine, kuti Inu muzindiwuza kuti ndiŵafungate pachifuwa panga, monga momwe mlezi amachitira poyamwitsa mwana, ndipo kuti ndipite nawo ku dziko limene mudalonjeza makolo ao molumbira kuti mudzaŵapatsa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Ndine amene ndinatenga pathupi pa anthu onsewa? Kodi ndinawabala ndine? Bwanji mukundiwuza kuti ndiwanyamule mʼmanja mwanga, monga momwe mlezi amanyamulira kamwana, kupita nawo ku malo omwe munalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi ndinaima nao anthu awa onse? kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kumka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?