Numbers 11:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Mose kuti, “Usonkhanitse amuna makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, anthu amene ukuŵadziŵa kuti ndi atsogoleri ndi akapitao a anthu. Ubwere nawo ku chihema chamsonkhano, ndipo aime kumeneko pamodzi ndi iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Mose kuti, “Undibweretsere anthu 70 ochokera pakati pa akuluakulu a Aisraeli, amene umawadziwa kuti ndiwo atsogoleri komanso akuluakulu a mabanja. Abwere ku tenti ya msonkhano kuti ayime kumeneko pamodzi ndi iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akuru a Israyeli, amene uwadziwa kuti ndiwo akuru a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku cihema cokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.