Numbers 11:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imeneyo mudzaidya mwezi wathunthu, mpaka izikachita kutulukira m'makutu, inuyo nkumadwala nayo. Zimenezi zidzachitika chifukwa choti mwakana Chauta amene amakhala pakati panu, ndipo mwadandaula pamaso pake nkumati, “Chifukwa chiyani tidatuluka ku Ejipito?” ’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji m'Ejipito?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma mwezi wonse, mpaka itakukolani ndi kutopa nayo chifukwa mwakana Yehova yemwe ali pakati panu ndipo mwalira pamaso pake kuti, ‘Bwanji tinachoka ku Igupto?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pace, ndi kuti, Tinaturukiranji m'Aigupto?