Numbers 11:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adatsika mu mtambo nayamba kulankhula ndi Mose. Ndipo adatengako mzimu umene unali pa Moseyo nauika pa akuluakulu makumi asanu ndi aŵiriwo. Anthuwo atalandira mzimu uja, adayamba kulosa. Koma sadapitirire kulosako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anatsika mʼmitambo ndi kuyankhula naye ndipo anatengako mzimu womwe unali pa Mose ndi kuwuyika pa akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja. Pamene mzimuwo unakhazikika pa akuluakuluwo, anayamba kunenera koma sanapitirize.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena nave, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akuru makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.