Numbers 11:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aŵiri adatsalira m'mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m'gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m'mahema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma amuna awiri anatsalira m'cigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzace ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanaturuka kumka kucihema; ndipo ananenera m'cigono.