Numbers 11:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mose adamuuza kuti, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikadakondwa anthu onse a Chauta akadakhala aneneri, ndipo Chauta akadaika mzimu wake pa iwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mose anati, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikanakonda kuti anthu onse a Yehova akhale aneneri ndi kuti Yehova ayike mzimu wake pa iwo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mose anati kwa iye, Kodi ucita nsanje nao cifukwa ca ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! mwenzi Yehova atawaikira mzimu wace!