Numbers 11:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adautsa mphepo kuchokera ku nyanja. Mphepoyo idabwera ndi zinziri, ndipo zidagwera pafupi ndi mahema. Kuchokera kumahemako, zinzirizo zidagwa pa mtunda woyenda ulendo wa tsiku limodzi mbali imodzi, mbali inanso chimodzimodzi, mozungulira mahemawo. Zitaunjikana, mjintchi wake unali ngati mita limodzi kuchokera pansi mpaka pamwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zochokera kunyanja, nizitula kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudacokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zocokera kunyanja, nizitula kucigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa cigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.