Numbers 11:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu atadzuka, ankagwira zinzirizo masana onse ndi usiku. M'maŵa mwakenso tsiku lathunthu, adachita chimodzimodzi. Panalibe ndi mmodzi yemwe amene adagwira zinziri zochepera makilogaramu chikwi chimodzi. Ndipo adaziyanika kuzungulira mahema onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wace wonse, ndi mawa lace lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa cigono.