Numbers 11:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyama ikadali m'kamwa mwao, asanaimeze nkomwe, Chauta adaŵapsera mtima anthuwo, ndipo adaŵagwetsera mliri woopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene anthuwo ankadya nyamayo, asanayimeze nʼkomwe, ukali wa Yehova unafika pa iwo ndipo Iye anawakantha ndi mliri woopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukuru ndithu.