Numbers 11:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ankapita kukatola manayo, namapera pa mphero kapena kusinja mu mtondo, ndipo ankaphika, namapangira makeke. Kukoma kwake kunali ngati makeke ophika ndi mafuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu amamka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.