Numbers 12:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta adauza Mose kuti, “Bambo wake akadamthira malovu kumaso, kodi Miriyamu sakadachita manyazi masiku asanu ndi aŵiri? Basi, amtsekere kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake angathe kumloŵetsanso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayankha Mose kuti, “Abambo ake akanamulavulira malovu mʼmaso, kodi sakanakhala wonyozeka masiku asanu ndi awiri? Mutsekereni kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri, kenaka mumulowetsenso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wace akadamlabvulira malobvu pankhope pace sakadacita manyazi masiku asanu ndi awiri? ambindikiritse kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.