Numbers 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikupatsa Aisraele. Pa fuko lililonse utume munthu mmodzi, amene ali mtsogoleri m'fukolo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndirikupatsa ana a Israyeli; utumize munthu mmodzi wa pfuko liri lonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzace.