Numbers 13:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukaonenso ngati dzikolo ndi lolemera kapena losauka, ndipo ngati nkhalango zilimo kapena ai. Mulimbe mtima, ndipo mukabwere ndi zipatso zina zam'dzikomo.” Imeneyo inali nyengo yopsa mphesa zoyamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi umo iliri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe. Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi umo iriri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe, Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.