Numbers 13:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adadzera njira ya ku Negebu nakafika ku Hebroni, kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. (Adamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri asanamange Zowani ku Ejipito.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani m'Ejipito.)
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakwera njira ya kumwela nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talmai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zoani m'Aigupto.)