Numbers 13:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵauza kuti, “Tidakafika kudziko kumene inu mudatituma. Dzikolo ndi lamwanaalirenji, zipatso zake ndi izi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafotokozera, nati, Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu a moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndi zipatso zace siizi.