Numbers 13:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu anthu am'dzikomo ngamphamvu, mizinda yao ndi yozingidwa ndi malinga, ndiponso ndi yaikulu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, tidaonanso zidzukulu za Aanaki kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikuru ndithu: ndipo tinaonakonso ana a Anaki.