Numbers 13:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Kalebe adaŵakhalitsa chete anthu pamaso pa Mose, nati, “Tiyeni tipite nthaŵi yomwe ino, tikalande dzikolo, chifukwa tingathe kuligonjetsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Kalebi anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathu lathu; popeza tikhozadi kucita kumene.