Numbers 13:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adasimbira Aisraelewo zoipa za dzikolo zimene adakaziwona, adati, “Dziko limene tidakalizondalo ndi dziko limene limaononga anthu ake. Ndipo anthu onse amene tidaŵaona kumeneko ngaataliatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaipsira ana a Israele mbiri ya dziko adalizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaipsira ana a Israyeli mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pace ndiwo anthu atali misinkhu.