Numbers 14:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi anthu ameneŵa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzaleka liti kusandikhulupirira, ngakhale aone zizindikiro zimene ndachita pakati pao?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Mose kuti, “Anthu awa adzandinyoza mpaka liti? Sadzandikhulupirira mpaka liti, ngakhale ndachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi pakati pawo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, cinkana zizindikilo zonse ndinazicita pakati pao?