Numbers 14:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Yehova sakwiya msanga, ndipo ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika, wokhululukira tchimo ndi kuwukira. Koma Iye sadzaleka kulanga ochimwa. Iyeyo amalanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo kufikira mʼbado wachitatu ndi wachinayi.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova ndiye wolekereza, ndi wa cifundo cocuruka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula woparamula; wakuwalanga ana cifukwa ca mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai.