Numbers 14:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukupemphani kuti muŵakhululukire kuchimwa kwao anthu ameneŵa kaamba ka chifundo chanu chachikulu ndi chosasinthika, ndiponso chifukwa mwakhala mukuŵakhululukira anthu ameneŵa kuyambira ku Ejipito mpaka tsopano lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, akhululukireni anthuwa tchimo lawo monga mwakhala mukuwakhululukira kuchokera pa nthawi imene anachoka ku Igupto mpaka tsopano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa cifundo canu cacikuru, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Aigupto kufikira tsopano.