Numbers 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele onse adayamba kuŵiringulira Mose ndi Aroni. Mpingo wonse udaŵauza kuti, “Kukadakhala bwino tikadangofera ku Ejipito, kapena m'chipululu mommuno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana onse a Israyeli anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m'cipululu muno!