Numbers 14:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dzikolo. Anthu ameneŵa adaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga zimene ndidachita ku Ejipito ndi m'chipululu muno, komabe adandipenekera kakhumi konse osamvera mau anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita m'Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinazichita ku Igupto ndi mʼchipululu muno, koma osandimvera ndi kundiyesa kokwanira kakhumi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikilo zanga, ndidazicita m'Aigupto ndi m'cipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;