Numbers 14:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitembo yanu idzakhala ili ngundangunda mʼchipululu muno; mtembo wa munthu aliyense pakati panu amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, amene anawerengedwa pa chiwerengero chija ndipo anangʼungʼudza motsutsana nane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwanu konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;