Numbers 14:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Padzapita zaka makumi anai mukulangidwa chifukwa cha zolakwa zanu, kuŵerenga chaka chimodzi pa tsiku lililonse la masiku makumi anai aja amene munkazonda dziko. Mudzadziŵa kuwopsa kwake kwa kukangana ndi Ine.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzavutika chifukwa cha machimo anu kwa zaka makumi anayi Chaka chimodzi chikuyimira tsiku limodzi la masiku makumi anayi amene munakazonda dziko lija ndipo mudzadziwa kuyipa kwake kwa kukangana ndi Ine.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga caka cimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.