Numbers 14:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalaŵirira m'mamaŵa, ndipo adakwera cha ku dziko lamapiri, nati “Ife pano takonzeka kukwera mpaka kukafika ku malo amene Chauta adatilonjeza. Ndithu tachimwadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba pa phiri, nati, Tili pano, tidzakwera kunka ku malo amene Yehova ananena; popeza tachimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmamawa tsiku linalo anapita mbali ya ku dziko la mapiri. Iwo anati, “Tachimwa, tipita ku dziko limene Yehova anatilonjeza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba pa, phiri, nati, Tiri pano, tidzakwera kumka ku malo amene Yehova ananena; popeza tacimwa.