Numbers 15:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati ndi mlendo amene akhala pakati panu, kapena wina aliyense amene akhala pakati panu pa mibadwo yanu yonse, ndipo afuna kupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta, azichita monga momwe muchitira inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena ali yense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakacitira Yehova nsembe yamoto ya pfungo lokoma; monga mucita inu, momwemo iyenso,