Numbers 15:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati cholakwacho chidachitika mosadziŵa, mpingo womwe osazindikira, pamenepo mpingo wonsewo upereke mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Apereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chakumwa, potsata zimene ndidakulamulani. Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo kudzali, ngati anacicita osati dala, osacidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya pfungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira, monga mwa ciweruzo cace; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo.