Numbers 15:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a mpingo wonse wa Aisraele ndipo anthuwo adzakhululukidwa, chifukwa choti adalakwa mosadziŵa. Tsono atabwera ndi zopereka zao ngati nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, ndiponso ngati nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta, kuti azimpepesa pa cholakwa chao chija,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe azicita cotetezera khamu lonse la ana a Israyeli, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanacita dala, ndipo anadza naco copereka cao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yaucimo pamaso pa Yehova, cifukwa ca kulakwa osati dala.