Numbers 15:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu amene achimwa dala, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, wanyoza Chauta, ndipo munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma munthu wakucita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo acitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wace.