Numbers 15:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mphonje imeneyo muzidzaiyang'ana ndi kumakumbukira malamulo onse a Chauta, kuti muziŵamvera, ndipo musamatsatenso zilakolako zokhota za mtima wanu kapena za maso anu zimene munkazitsata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukila malamulo onse a Yehova, ndi kuwacita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi cigololo;