Numbers 15:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amene adzabwere ndi zoperekayo, adzapereke kwa Chauta chopereka cha chakudya, cholemera kilogaramu limodzi, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo iye wobwera naco copereka cace kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la bini la mafuta;