Numbers 15:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mupereka ng'ombe yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yopsereza kapena nsembe yopembedzera, kapena kuti zichitikedi zimene mudalumbira, kapena kuti ikhale nsembe yachiyanjano,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kucita cowinda ca padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;