Numbers 16:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mose adapsa mtima kwambiri, ndipo adauza Chauta kuti, “Musalandire nsembe za anthu ameneŵa. Sindidaŵalande ndi bulu mmodzi yemwe, ndipo sindidalakwire ndi mmodzi yemwe mwa iwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalanda bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira copereka cao; siodinalanda buru wao mmodzi, kapena kucitira coipa mmodzi wa iwowa.