Numbers 16:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza mpingowo kuti, “Ndapota nanu, chokani pakati pa mahema a anthu oipaŵa, ndipo musakhudze chinthu chao chilichonse, kuti angakuphereni kumodzi chifukwa cha zoipa zao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Cokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kali konse, mungaonongeke m'zocimwa zao zonse.