Numbers 16:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adati, “Pano muzindikira kuti ntchito zonse ndikuchitazi, adandituma ndi Chauta, si za m'mutu mwanga ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwangamwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mose anati, “Umu ndi mmene mudzadziwire kuti Yehova ndiye amene anandituma kuti ndichite zinthu zonsezi ndipo kuti si maganizo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati, Ndi ici mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kucita nchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwanga mwanga.