Numbers 16:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta akachita chinthu china chachilendo, nthaka ikayasama ndi kuŵameza iwowo pamodzi ndi zinthu zao zonse, natsikira kumanda ali moyo, mpamene mudziŵe kuti anthu ameneŵa anyoza Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova akalenga cinthu catsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pace, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.