Numbers 16:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti zikhale chikumbutso kwa Aisraele, kuti munthu aliyense amene sali wansembe, amene sali mmodzi mwa zidzukulu za Aroni, asayandikire kudzafukiza lubani pamaso pa Chauta, kuti zingamgwere zonga zimene zidagwera Kora ndi gulu lake. Zonse zidachitika monga momwe Chauta adauzira Eleazara kudzera mwa Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
monga momwe Yehova anamulangizira kudzera mwa Mose. Chimenechi chinali chikumbutso kwa Aisraeli kuti munthu wina aliyense, kupatula zidzukulu za Aaroni, sayenera kupsereza lubani pamaso pa Yehova, kuopa kuti munthu woteroyo angakhale ngati Kora ndi omutsatira ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cikhale cikumbutso kwa ana a Israyeli, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kucita cofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lace; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.