Numbers 16:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mpingo udasonkhana kuti uukire Mose ndi Aroni, anthuwo adatembenuka ndi kuyang'ana ku chihema chamsonkhano. Tsono adangoona mtambo utaphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anaceukira cihema cokomanako; taonani, mtambo unaciphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.