Numbers 16:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza Aroni kuti, “Tenga chofukizira lubani chako, ndipo uikemo moto wa pa guwa ndi kuthiramo lubani. Upite nacho msanga kumene kuli gulu la anthuko, ndipo uŵachitire mwambo wopepesera machimo ao. Inde, mkwiyo wa Chauta watsika, ndipo mliri wayamba kale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo moto wa ku guwa la nsembe, nuikepo chofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwachitire chowatetezera; pakuti watuluka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Tenga chofukizira chako ndipo ikamo lubani pamodzi ndi moto wochokera pa guwa lansembe, fulumira, pita pa gulu la anthuwo ndipo ukachite nsembe yopepesera machimo awo popeza mkwiyo wa Yehova wafika, mliri wayamba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo mota wa ku guwa la nsembe, nuikepo cofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwacitire cowatetezera; pakuti waturuka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.