Numbers 16:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Aroni adatenga chofukizira, nathamangira pakati penipeni pa msonkhano. Ndipo adangoona mliri utayamba kale pa anthuwo. Tsono adathira lubani, nachita mwambo wopepesera machimo a anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo cofukiza nawacitira anthu cowatetezera.